Headline

The Hotel, Food Processing and Catering Workers Union, was established with an aim to promote Industrial Peace in various companies in the sector.

UNION ? MTENDERE PA NTCHITO

1.Kodi Trade Union Nchiyani?

 

Trade Union ndi bungwe lokhazikitsidwa ndi anthu ogwira ntchito ndi cholinga choteteza, kuthandiza ndi kukwaniritsa ufulu wa anthu ogwira ntchito. Kumbukirani kuti anthu olemba ntchito anzawo mdziko muno alinso ndi awo mabungwe monga ECAM komanso Chamber of Commerce.

 

2.Kodi ma Trade Union ndi oloredwa mdziko muno?

 

INDE: Ufulu wa anthu ogwira ntchito, ndi mabungwe owayimira, ndi obvomerezedwa pa malamulo a dziko lino, komanso m’buku la malamulo a chaka cha 1996 ndipo malamulo amenewa ndi ofanana ndi onse a padziko lapansi onena za ufulu wachibadwidwe komanso ufulu wa oguira ntchito ndi mabungwe oyimira ogwira ntchito.

 

3.Kodi Trade Union ingandichitire chiyani?

 

ZAMBIRIMBIRI, monga life insurance komanso kukuthandizani pa ntchito yanu pakuonetsetsa kuti mudzalandira malipiro oyenera muli pa ntchito kapenanso mutasiya. Union idzaonesetsa kuti mudzilandira malipiro oyenera muli pa ntchito kapenanso mutasiya. Union idzaonetsetsa kuti olemba anzawo ntchito akusamala bwino olembedwawo pogwirizana pa za malipiro abwino a wanthu ogwira ntchito, malamulo abwino a pantchito, ukhondo komanso zina ndi zina zofunika munthu pa ntchito. Zonsezi munthu olembedwa ntchito sangamvere ayi omulembawo, ndichifukwa chake mukalowa mu Union, ndi Union imene idzakuimilireni inu pokambirana ndi okulembaniwo.

 

4.Kodi ma Trade Union sagwirizana ndi olemba ntchito?

 

AYI, sizoona zimenezo ma Union ndi olemba anthu ntchito ndi amodzi pa chitukuko china chiri chonse. Eni ntchito ali ndi ma business ndipo amakhala ndi ndalama pa Business zawo koma olembedwa ntchito ndikuonetsa luso ndi khama pa ntchitoyo. Popanda olemba anzawo ntchito ndiye kuti ntchito kulibe komanso popanda olembedwa ntchito ndiye kuti business kulibenso. Onsewa ayenera kugwira ntchito limodzi kuti zonse ziyende bwino. Olembedwa ngati ali ndi bungwe lawo, zonse zimakhala bwino chifukwa ndi bungwelo lomwe limakambirana ndi mabwana poletsa zina monga kunyanyala ntchito (strike) kapena kuchotsedwa popanda cholakwika.

 

  1. Kodikusiyana pakati pa Trade Union ndi JCC kuli pati?

 

Trade Union ndi bungwe lodziimira pa lokha lokhazikitsidwa ndi olembedwa ntchito pamene ma JCC’s ndi okhazikitsidwa ndi olemba anzawo ntchito komanso mumapezeka ena oimira olembedwa ntchito. Ma JCC’s siothandiza konse komanso palibe olembedwa ntchito adaonapo phindu lake. Pa malamulo a m’dziko lino komanso pa malamulo apa ntchito, ma JCC’s alibe mphamvu ngati ma Trade Union pa kuimilira anthu olembedwa ntchito mdziko muno.

 

  1. Kodi ndingalowe nawo Trade Union?

 

Musadikire kukumana ndi mabvuto monga kuchotsedwa ntchito, kusalipiridwa, kumanidwa ndalama za Holiday (leave grant) komanso penshoni. Ngati muli ndi Life Insurance, zikutanthauza kuti simudadikire kufa kuti kukhale nawo. Pachifukwa ichi, konzekelanitu tsogolo lanu. Trade Union ndi ma Insurance a ntchito yanu. Aliyense ogwira ntchito ali ndi ufulu wolowa mu Trade Union lero.

 

  1. Kodi amene adandilemba ine ntchito angandiletse kulowa mu Trade Union?

 

Olemba anthu ntchito amafunitsitsa atamauza olembedwawo kuti ma Trade Union ndi oyipa chifukwa amadziwa kuti aliyense ogwira ntchito payekha sangadziteteze pa zobvuta zake oa ntchitopo. Dziwani kuti chala chimodzi si chiswa nsabwe, mgwirizano ndi ofunika. Olembedwa ntchito amene adalowa Union ndi otetezedwa bwino kusiyana ndi amene Sali mamembala komanso ndi kuphwanya malamulo a dziko lino ngati munthu aletsedwa kulowa Union.

 

  1. Kodi ndingalowe bwanji Trade Union?

 

Zosabvuta: Kuti mukhale membala, lembani zonse zoyenera pa fomu imene mudzapatsidwe komanso funsani kwa Organiser wa Union amene adzakupatseni fomu pa nthawi imene inu mudzafuna kulowa union.

 

  1. Olemba anthu ntchito akuletsa otiyang’anira komanso ma manijala kuti asalowe mu Union ati chifukwa ndi olamulira?

 

Izi zingatheke, koma okuyang’anirani inu pa ntchito alibe mphamvu yochotsa anthu pa ntchito, kukweza kapena kumutsitsa munthu pa ntchito kapenanso alibe mphamvu yakayendetsedwe ka ntchito m’malo mwa Company kapena eni ake a ntchito, amenewo akhoza kulowa Union chifukwa alibe mphamvu zenizeni za u manijala. Dziwani kuti aliyense ogwira ntchito ali ndi ufulu olowa Trade Union.

 

  1. Trade Union ndi Bungwe lomwe likuonesetsa kuti ufulu wa democracy ukutsatidwa m’dziko muno komanso bungweli limatenga nawo mbali pa zokambirana zopititsa m’tsogolo ufulu wachibadwidwe.

 

  1. Trade Union ndi Bungwe lomwe likuyesetsa kuphunzitsa anthu kuti adziwe ufulu wawo powadziwitsa njira yakupewa umbuli, umphawi ndinso matenda komanso kuonesetsa kuti anthu azilandira nalipiro abwino pa ntchito pokambirana ndi Boma ndi ma bungwe ena am’dziko muno komanso kunja kwa dziko lino.

 

  1. Trade Union ndi Bungwe lomwe litha kukuimilirani inu pa milandu yanu ku khoti komanso kutsutsana ndi anthu owagwilira ntchito.

 

MU UMODZI MULI MPHAMVU